Malawi News

Anthu adzilankhulabe za imfa ya Chilima – Chirwa

Anthu adzilankhulabe za imfa ya Chilima – Chirwa

Katswiri pa nkhani za ndale, Thomas Chirwa, yemwenso ndi mphunzitsi pa sukulu ya ukachenjede ya (University of Dar Es Salaam) koma ndi M’malawi wati ndipovuta kuti andale azipani zotsutsa asiye kumayankhula za imfa ya yemwe adali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima pa misonkhano yawo.


Chirwa wati ngati anthu akuyankhula kwambiri nkhani yokhudza imfa ya a Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu ndiye kuti boma lalephera kuwafotokera a Malawi zogwirika. 


“Boma ndilomwe likupangitsa kuti anthu azikamba za nkhaniyi. Mukudziwa inu kuti mtsogoleri wadziko lino Lazarus Chakwera adauza mtundu wa a Malawi kuti ndege anachita kuibwenza ku Mzuzu italephera kutera pa bwalo la ndege la Mzuzu, pomwe ripoti loyembekezera la akatswiri omwe amafufuza za ngozi ya ndegeyo aku German, anatsindika kuti ndegeyo sinafike ku Mzuzu, ichi ndi chitsanzo chimodzi cha zomwe anthu sangakhulupirire boma pa nkhaniyi.


Chilima
Chirwa: Anthu sakukhulupilira zomwe boma lidanena.

Pa pempho lomwe mkazi wa malemu a Chilima, Mary Chilima anapempha a Malawi kuti awathandize kupeza chilungamo podziwa zenizeni zomwe zinachitika kuti amuna awo amwalire, iwo ati: “Mau omwe a Mary Chilima ananena zikusonyezeratu kuti sakukhutira ndi kafukufuku yemwe boma lidachita podzera kwa azakafukufuku ochokera ku German,” watero Chirwa.


Katakweyu wawuzanso Malawi24 kuti ndi wodabwa kuti mpaka pano boma silinakhazikitse komiti yapadera (Commission of Enquiry) yoti iwunguze zomwe zinachitika, iye wati komitiyo mukuyenera kukhalamo aku mawanja aanthu omwe anamwalira, atsogoleri azipani zonse komanso akumabwalo amilandu ndi ena otero.


Nduna yazofalitsa nkhani Moses Kunkuyu idauza a Malawi kuti boma lili ndi chikhulupiliro ndi azakafukufuku aku German ndipo ndikofunika kuti a Malawi adikire ripoti yonse.


Ndunayi inatinso malamulo akakhazikitsidwe ka komiti ya zofufuzafufuza


Posachedwapa a Chakwera adauza anthu pa msonkhano omwe unachitika ku Zomba kuti azipani zotsutsa asapangirepo ndale pa imfa ya Chilima ndi anthu ena asanu ndi atatu, omwe anamwalira pa 10 June 2024 pa ngozi ya ndege mumapili a Chikangawa ku nthungwa m’boma la Mzimba.