Mchithunzi powona zitha kumawoneka ngati ndi yawo njinga koma ayi, a Dalitso Peter ali m’manja mwa apolisi ku Lilongwe chifukwa choba njinga yamoto komanso kusunga munthu wina mokakamiza.
Oyankhulira polisi ya Lilongwe, a Hastings Chigalu, ati a Peter omwe ndi a zaka 28 limodzi ndi anzawo ena awiri adaba njinga ndi kupatsa munthu wina kuti akawagulitsire pa mtengo wa 500, 000 kwacha, zomwe zinadabwitsa mfumu ina yokhala moyandikira sukulu ya ukachenjede ya NRC m’boma lomweli.
Malinga ndi a Chigalu mfumuyi idalangiza ogulitsayu kuti akatule njingayi ku polisi itadabwa ndi kuchepa kwa mtengo ogulitsira.
“Oganizilidwawo atawona kuti nkulu okagulitsa njinga sakubweretsa ndalama kapena njinga, anagwira mng’ono wake ndi kukamusunga mokakamiza ku malo otchedwa Diamphwi,” anatelo a Chigalu.
A Chigalu anawonjezera kuti oganizilidwawa limodzi ndi anzawo anayamba kuwopsyeza abale ake a yemwe anampatsira njinga kuti akapanda kubweza ndalama kapena njinga iwo apha mchimwene wawo yemwe anamugwirayo.
Abale a wongwidwayo adatengana ndi a chitetezo cha m’mudzi ndikutsatira anthuwa povomeleza kukawapatsa ndalama, ndipo iwo anakwanitsa kugwira a Peter ndipo anzawo awiri anathawa.
A Dalitso Peter amachokera m’mudzi mwa a Geya m’boma la Salima.
0 Comments