Malawi News

Amuna ambiri akudzipha m’dziko muno

Amuna ambiri akudzipha m’dziko muno

Apolisi ati chiwelengero cha amuna amene akudzipha okha m’dziko muno chikukwera kwambiri.


Malingana ndi lipoti limene atulutsa akulikulu la apolisi ku Lilongwe, amuna okwana 246 achotsa miyoyo yawo kuyambira mu mwezi wa January kufika June chaka chino ndipo akazi okwana 35 ndi omwe adzipha munyengo yomweyi.


Wachiwiri kwa ofalitsa nkhani za polisi m’dziko muno a Harry Namwaza ati chiwelengelochi ndi chokwera kusiyanitsa ndi chaka chatha mu nyengo ngati yomweyi pomwe amuna 198 komanso akazi 22 anazipha.


Poyankhula ndi Malawi24, a Namwaza anati pali zifukwa zingapo zomwe zikupangitsa kuti anthu m’dziko muno azipanga mchitidwewu.


“Imfa ngati izi zikuchitika chifukwa cha ngongole, nkhawa, mavuto a m’banja komanso mchitidwe ogwiritsa kwambiri mankhwala osokoneza ubongo omwe wakula pakati pa achinyamata,” adafotokoza a Namwaza.


Iwo anati imfa za mtundu uwu ndi zokhumudwitsa kwambiri ndipo apempha onse amene akukumana ndi nkhawa komanso mavuto osiyanasiyana kuti adzitula nkhawa zawo kwa anthu omwe amawakhulupilira m’malo moganiza zongodzipha.


A Namwaza apemphanso mabungwe komanso anthu akufuna kwabwino m’dziko muno kuti alimbikitse ntchito yopeleka mauthenga okhudza matenda a muubongo kuti mchitidwewu uchepe m’dziko muno.