Malawi News

Abambo atatu anjatidwa powaganizira kuti ndiakuba ku Lilongwe

Abambo atatu anjatidwa powaganizira kuti ndiakuba ku Lilongwe

Apolisi ku Lilongwe amanga abambo atatu omwe akuwaganizira kuti akhala akuba m’mashopu ndi m’manyumba osatha kumanga ku dera la Chitipi.


Malingana ndi wachiwiri kwa m’neneri wa polisi ya Lilongwe, a Khumbo Sanyiwa, anthuwa anaba ma belo a sugar, zitseko, mafosholo, ma felemu azitseko, ndi matumba achimanga mwazina, zokwana K3.4 million.


Zadziwika kuti anthuwa ndi a Stephano Maganga a zaka 27, Harward Chikumbutso a zaka 30 ndi a  Frank Ezalias a zaka 31.


Malingana ndi a Sanyiwa, apolisi apa Chitipi ndi amene akwanita kugwira abambowa atachita kafukufuku wamphavu pa za nkhaniyi ndipo wina mwa katundu obedwayo wapezeka.


Pakali pano, apolisi adakachitabe kafukufuku ndi cholinga choti agwire anthu ena omwe akukhudzidwa ndi nkhaniyi ndikupeza katundu wina obedwa pothyola nyumba m’madera a Chinsapo, Chitipi ndi Njewa mwa ena.