Malawi News

Abambo achikulire omwe akuganiziridwa milandu yakupha apatsidwa belo

Abambo achikulire omwe akuganiziridwa milandu yakupha apatsidwa belo

Abambo asanu achikulire omwe amaganizilidwa milandu yakupha ndipo milandu yawo sidayambe kumvedwa patantha nthawi yaitali, alamulidwa ndi bwalo lalikulu ku Zomba kuti atuluke ndikukadikila za milandu yawo kunyumba.


Abambowa akhala akusungidwa ku ndende yaikulu ya Zomba ndipo amakhala mbali ina ya ndendeyi komwe kumakhala achikulire okhaokha.


Malingana ndi Legal Aid Bureau, chiwamangireni anthuwa milandu yawo siidayambe kumvedwa.


“Zitadziwika kuti pali abambo achikulire omwe akufunika thandizo ku ndendeyi, Legal Aid Bureau kudzera mwa Assistant Director waku Zomba, Zaheed Ndeketa, inapita kukawazonda. Zitatero, milandu yawo inatengedwa ndi Legal Aid Bureau ndipo kubwalo lamilandu amawathandiza ndi a Ndeketa,” yatsindika motero Legal Aid Bureau.


Anthuwa atuluka pa belo ndipo maina aabambowa ndi a Jim Kalunga azaka 84 zakubadwa ndipo anamangidwa pa 23 July 2023, a James Kabish komanso Master Michael omwe anamangidwa mu May chaka cha 2022, a Mayeke Julius omwe anamangidwa mu November 2022, komanso a Witness Kambona omwe anamangidwa mchaka cha 2011.