Malawi News

Zipani ziwiri zikuluzikulu zinandipempha kuti ndikhale runningmate ine ndidakana – Bushiri

Zipani ziwiri zikuluzikulu zinandipempha kuti ndikhale runningmate ine ndidakana – Bushiri

Mtumiki Shepherd Bushiri wati zipani ziwiri zikuluzikulu m’dziko muno zinamupeza ndikumupempha kuti akhale wachiwiri kwa otsogolera zipanizo (running mate), koma iye anakanitsitsa kuti sakufuna kupanga zimenezo. Iwo afotokoza izi mu macheza awo ndi kanema wa Zodiak.


A Bushiri awuza kanemayu kuti anakana pempholo chifukwa choti samapanga za ndale ndipo si munthu wandale.


“Anandipeza ndithu ndikupempha kuti ndikakhale running mate koma ine ndinakana,” Iwo anatero.


Atafunsidwa kuti zipani zake ndi ziti, a Bushiri anakana kutchula mayina a zipanizo. Koma mukulakhura kwawo iwo atsindika kuti zipanizo ndi zikuluzikulu m’dziko muno.


Pakalipano zipani zomwe zili zikuluzikulu kuno ku Malawi ndi DPP ndi MCP.