Malawi News

Tiyembekezere mvula mwezi wa October – DCCMS

Tiyembekezere mvula mwezi wa October – DCCMS

Nthambi yoona za nyengo m’dziko muno ya Department of Climate Change and Meteorological Services (DCCMS) yati mu mwezi wa October, madera ambiri akuyembekezereka kulandira mvula yamlingo okhazikika kapena kuposera apo.


DCCMS yati nyengo ya dzinja ku Malawi kuno imayamba mu October kufikira m’mwezi wa April ndipo nyengoyi imakhazikika m’mwezi wa November kuyambira kumwera kwadziko lino ndipo pang’ono ndi pang’ono kumafikira m’zigawo zapakati komanso kumpoto.


“Mvula ya Chizimalupsya ndiyomwe imayambilira nyengo yadzinja isanakhazikike. Mu mwezi wa October, madera ambiri mdziko muno akuyembekezereka kulandira mvula yamlingo okhazikika kapena kuposera apo.


“Komabe, madera ambiri a chigawo chapakati, mphepete mwa Nyanja ndi kumpoto akuyembekezereka kulandira mvula yoposera mlingo okhazikika. Mlingo wamvulawu ukhala wapafupifupi 50mm mu mweziwu,” yatero DCCMS.


Ndipo polosera za m’mene nyengo ikhalire lero, nthambiyi yati kukhala kwa mphepo, kwa mitambo ndipo kugwa mvula makamaka m’madera am’chigawo cha kum’mwera ndi am’mphepete mwa nyanja ya Malawi. 


Ndipo m’mawa wa pa 2 October, temperature ili pa 12°C ndipo masana idzakhala pa 31°C.


Nthambiyi yatinso mphepo ya Mwera iwombanso pa nyanja ya Malawi ndi nyanja zina kuyambira usiku wa Lachiwiri pa 1 October, 2024.