Public Affairs Committee (PAC) yalimbikitsa zipani kuti zizichita kampeni ya mtendere pamene dziko la Malawi likuyembekezeka kuchititsa zisankho zapatatu pa 16 September chaka chino.
Izi zadziwika Lachinayi pamene PAC idakumana ndi mtsogoleri wa chipani chotsutsa cha Democratic Progressive (DPP), a Arthur Peter Mutharika kunyumba kwawo m’boma la Mangochi.
Motsogozedwa ndi wapampando wa komitiyi Monsinyu Patrick Thawale, PAC yati pali kufunika kochita zinthu mwamtendere ndikupewa ziwawa zomwe zimadza pamene andale akuchita kampeni yonyozana.
Komitiyi idatinso ndikwabwino kuti pazikhala zokambirana zamtendere ndi njira zopewera mikangano ngati pali kusiyana maganizo.
M’mawu awo a Mutharika adagwirizana ndi mawu a komitiyi pakufunika kwa mtendere ndi chilungamo mu ndondomeko zonse za chitsankho.
A Mutharika adatinso ndikofunika kuti komitiyi igwirane manja ndi zipani zotsutsa zomwe zikufuna kuti chilungamo cha m’mene ntchito yolemba ndi kuyendetsa chitsankho ikuyendera kamba koti kuchita ntchitoyi mosabisa kalikonse ndikofunikira kuti chitsankho chidzayende bwino.
Iwo anati chipani chawo sichidzalora kuti zachinyengo zilizonse zomwe chipani cholamula cha Malawi Congress (MCP) chikukonza zichitike pa zisankhozi.
0 Comments