Otsatira chipani chotsutsa cha Democratic Progressive Party (DPP) asonyeza kudabwa ndi kukhudzidwa ndi kusunthidwa kwa gavanala woyang’anira ntchito za chipanichi m’chigawo cha pakati m’boma la Mangochi, a Sanudi Sande.
A Sande awasuntha pamene zokonzekera masankho a chipulula a chipani cha DPP zayandikira m’chigawo cha ku m’mawa. Kusunthidwaku kwadza kutsatira kukwezedwa udindo kuchoka pa gavanala a dera kufika pa wachiwiri kwa mlembi woyang’anira ntchito za chipanichi m’chigawo chakummawa (Deputy Organizing Secretary).
Malingana ndi zomwe tapeza kuchokera kwa akulu akulu achipanichi, a Sande analandirapo kalata kuchokera kwa gavanala wa bomali, a Raphael Yohane yowachotsa udindo wawo wa dera la phungu (constituency) pa 1 April, 2025.
Koma akuti izi sizinatheke kaamba koti akuluakulu a chipanichi mderalo analowelera atakumana ndi mamulumuzana a chipanichi kuphatikizapo mlembi wa mkulu, a Peter Mukhito.
Pakadali pano, a Sande akana udindo watsopanowu koma chipanichi chaika kale a Alick Piasi ngati Constituency Gavanala wa derali.
Poyankhulapo, ena mwa makhansala asanu omwe akuyenera kukapikisana nawo pa masankho a chipululawa adandaula ndi zomwe zachitikazi, ponena kuti zabwera nthawi yolakwika ndipo zisokoneza chisankho popeza munthu watsopanoyu sakudziwa bwino lomwe anthu ovota kapena kuti ma delegates pa chingerezi.
“Tikuona kuti izizi zapangidwa dala pofuna kukwaniritsa zina zolinga zomwe akufuna. Zokonzekera masankhowa (kuona maina aanthu ovota) zikuyamba mawa pa 23 April, ku Liwonde ndipo masankho akuyamba pa 25 April, 2025 ndiye kutichotsera yemwe akudziwa mainawa tinene kuti zili bwino?” anadandaula chotero m’modzi mwa makhansalawa yemwe sanafune kutchulidwa dzina.
Ku derali ndi komwe kulinso a Victoria Kingstone ngati phungu wa ku Nyumba ya Malamulo yemwe akuyenera kupikisana ndi Roza Mbilizi omwe ankagwira ntchito ku bungwe lotolera misonkho la Malawi Revenue Authority (MRA).
0 Comments