Malawi News

Okonda a Chakwera yang’anani kumbali: a Malawi ochuluka akufuna APM abwelere

Okonda a Chakwera yang’anani kumbali: a Malawi ochuluka akufuna APM abwelere

N’kuthekadi kuti chitsime chimadziwika ndi chakuya pamene chaphwera, chifukwa a Malawi ochuluka akuti bola kwa Farao komwe kuja. Ulendo wa ku Kenani ati aulephera ndipo iwo ndi okonzeka kubwelera.


Mtsogoleri wa kale a Peter Mutharika akuoneka ali ndi chikoka chochuluka pakati pa a Malawi ndipo anthu ochuluka ati iwo pokaponya voti azangopita kukachonga pa a Mutharika.


Kufunsa maganizo kwa sabata limodzi kumene tsamba lino linachita kwaonetsa kuti unyinji wa mzika za dziko lino watsamwa ndi utsogoleri wa a Chakwera ndipo akufuna kuti a Mutharika ndi chipani chawo cha DPP zibwelerenso.


Kwa sabata la thunthu, tsamba lino linafunsa a Malawi kuti asankhe amene avotere pa chisankho cha September uno pa mpando wa mtsogoleri wa dziko. Pa mndandanda panali mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera, mtsogoleri wa chipani cha UTM a Dalitso Kabambe ndinso mtsogoleri opuma a Peter Mutharika ndinso ena omwe aonetsa chidwi ngati Ras Chikomeni ndi ena otero.


Mutharika Chakwera Kabambe
Bola kwa Farao komwe kuja

Anthu atangoyamba kumene kuponya maganizo awo, a Mutharika adayamba kutsogola ndipo a Chakwera adali achiwiri. Izi koma zidasintha pamene timatseka kauniuni wa maganizoyu pamene a Lazarus Chakwera anabwera pachitatu.


Anthu pafupi-fupi 40 sauzande ndiwo anapereka nawo maganizoyu. Pa anthu amenewa, anthu 10 pa 100 alionse ndiwo adalumbira kuti iwo azavotera a Chakwera kuti apitirize. A Kabambe a UTM anapeza anthu ochulukirapo owakonda amene, ndipo pa anthu 100 alionse anthu 23 ndiwo amati azawavotera. Koma mtsogoleri wa kale a Peter Mutharika ndiwo adaoneka ali ndi chikoka, pa anthu 100 alionse ndiye kuti anthu okwana 62 ndiwo amati azawavotera.


Mu ndemanga zawo, ena mwa anthu amene adapereka maganizo awo anadandaula ndi kukwera mitengo kwa zinthu komanso kuvuta kwa katundu wina monga mafuta a galimoto ngati zifukwa zimene iwo akufunira kuti a Mutharika abwelere pa mpando.


Mkulu wina ochita za malonda adanena kuti iye malonda ake asokonekera chifukwa cha ulamuliro wa a Chakwera. Iye anati mu chisankho cha 2020 anavotera a Chakwera chifukwa cha malonjezo awo koma akadadziwa, sakadachita ndithu chifukwa amupweteka.


“Bizinesi yanga idalowa pansi, ndalama siyikulimba, kokapikula zinthu pena kulibe ndipo zikakhalapo zikumakhala zotsika mtengo. Abwelerenso a Mutharika basi,” iye anatero.


Koma ngakhale a Mutharika ali ndi chikoka chotere, ena akuwakayikira ati kamba koti adathamangitsidwa pa mpando kale pomwe ena ati iwo akula.


“Ine ndiye voti yanga ndi ya Kabambe,” wina anathilira ndemanga. “Kubwenzera a Mutharika ndiye zokanikazo, a Chakwera nawo ndiye palibe chimene akudziwa. Abwere watsopano basi, Kabambe.”


Koma anthu okonda a Chakwera ati maganizowa alibe ntchito chifukwa anthu ozavotera a Chakwera sakangalika ndi Facebook.


“Zitayani nthawi ndi kuvota kwanu pano, eni voti ali m’midzi ndipo azavotera Chakwera,” wina anatero kenako kuponyera voti yake kwa Chakwera.


Koma katswiri wina wa za kafukufuku wati zimene zikuonekazi ngakhale kuti ndi zosatsimikizika zikugwirizana ndi zochitika zina mu dziko muno.


“Pazokha zotsatira izi sizodalirika, koma ukaona ndi momwe anthu nawo akuyankhulira, a chipani cha MCP akuyenera kuchita mantha,” anatero katswiriyu.


Iye anaonjezerapo kuti zionetsero zomwe anthu akhala akuchita zingoonetseratu kuti a Chakwera alibe chikoka kwenikweni.


“Kunena kuti ovota ali m’midzi ndi zoona inde koma mukaonetsetsa olo mu midzi anthu nawo sali okondwa ndi a Chakwera,” anatero.


Mu chaka chatha bungwe lina la kafukufuku la Afrobarometer linapeza kuti a Malawi ochuluka akufuna a Mutharika ndipo owatsata pa chikoka anali a Chakwera. Pa nthawiyi ndi kuti a Kabambe asanatenge udindo wa mtsogoleri wa chipani cha UTM.