Malawi News

Nzika yaku Rwanda ili mchitolokosi kamba koba galimoto

Nzika yaku Rwanda ili mchitolokosi kamba koba galimoto

A Emmanuel Ndagijimana omwe ndi nzika ya dziko la Rwanda ndipo ali ndi zaka makumi anayi (40), amangidwa ndi a Polisi m’boma la Dowa kaamba kowaganizira kuti adaba galimoto.


Malingana ndi mneneli wa polisi ya Dowa, a Alice Sitima, galimotolo ndi la ndalama zokwana K7,990.00 ndipo ndi la mtundu wa Honda Freed DA 10595. Zadziwika kuti mkuluyu adaliba chaka chatha m’mwezi wa March ku msasa wa Dzaleka ku Dowa.


“Pa tsikuli bamboyu adabwereka kwa dalaivala wa galimotolo atamunamiza kuti akufuna achite malonda pa msasawu koma atachita izi anathawa ndi galimotolo,” atero a Sitima.


Iwo anapitiliza kunena kuti dalaivala wa galimotolo ataona kuti mkuluyo sakubwera adayesa kumuimbila lamya koma panthawiyo siimapezeka.


Zitatero mwini galimotolo ndi dalayivalayo adakamang’ala ku polisi za kubedwa kwa galimotolo ndipo pakali pano a polisi agwira bamboyo ndikupeza galimotolo ku Mzuzu komwe lidagulitsidwa ndikusinthidwa nambala yake.