
M’neneri Shepherd Bushiri wati kugula kwa ndege ndi chimodzi mwa zifukwa zomwe dziko la South Africa lidamumangira pamodzi ndi mkazi wake ponena kuti sizimagwirizana ndi msinkhu wake. Iwo afotokoza izi mu gawo loyamba la macheza awo ndi Kanema wa Zodiak.
Iwo ati moyo wawo ndi banja lawo mdziko la South Africa udali ovuta ndipo ichi nchifukwa chake adaganiza zobwera kuno ku mudzi. Atafunsidwa kuti afotokoze momwe adapezekera m’dziko muno, a Bushiri adakanitsitsa mwa mtu wa galu kuti sangayerekeze kuwulura, ponena kuti awalore kuti izi adzafotokozebe chifukwa ati nthawi imene m’nyumba mukuyaka moto, sulimbana ndi zambiri koma kuyang’ana pomwe pali mpata oti uthawire ndikupulumutsa moyo.
A Bushiri anapitiliza kufotokoza kuti ali m’dziko la South Africa, iwowo adapulumuka ku zipolopolo 47 kamba kakuti galimoto yawo idali ndi zipangizo zowakha zipolopolozo komanso iwo ndi akazi awo adapulumuka ku bomba lomwe ena kumeneko adatchera pa galimoto yawo.
Iwo ati imodzi mwa nkhaza zomwe dziko la South Africa lidachitira mneneriyu ndi banja lake ndi za imfa ya mwana wake oyamba, Israela, yemwe adakanizidwa kukalandira thandizo lamankhwara m’dzikomo ndipo atamutumiza kuno, nthumwi zina za m’dzikomo zidalembera kalata a Steven Kayuni yemwe pa nthawiyo adali mkulu oyimira boma pozenga milandu kuti mwanayu asaloledwe kupita m’dziko la Kenya kuti akalandire thandizolo kufikira pomwe adatsikira kulichete.
Iwo atinso anthu awiri omwe ankatumikira nawo limodzi adaomberedwa ndi kuphedwa ndipo ataona izi, adadziwa kuti njira yokhayo yopulumutsa moyo wawo ndikubwelera ku mudzi.
M’neneriyu, yemwe akuti amapanga ma business, sanafotokoze bwino bwino komwe ma business’wa ali, kuphatikizapo sukulu ya Ukachenjede yomwe akuti inatsekedwa ndi dziko la South Africa komwenso adasiya ndege yake.
Mneneriyu, yemwe akumanga mzinda wa Goshen ku Mangochi, sadalekeze pomwepo koma kuchenjeza onse omwe amadzitama nkuipitsa mbiri yawo pa masamba a mchezo kuti chaka chino chokha sawasekelera ndipo athana nawo ponena kuti aliyense opezeka akupanga izi, adzikapereka umboni ku bwalo lozenga milandu.
0 Comments