
Mtsogoleri wakale wa dziko lino, Joyce Banda wati pa mgwirizano wa Tonse Alliance, iwo adali mboni pamene mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera ndi wachiwiri wawo wakale malemu Saulos Klaus Chilima amagwirizana kuti aliyense adzalamulira zaka zisanu ngati mtsogoleri wa dziko lino.
Polankhula ndi kanema wa Zodiak, Mayi Joyce Banda anati aChilima anabwera kwa iwo kudzafunsa pamene adaona aChakwera akukakamila kuimilanso.

“Ine ndinali mboni pamene mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera ndi wachiwiri wawo wakale malemu Saulos Klaus Chilima amagwirizana kuti aliyense adzalamulira zaka zisanu ngati mtsogoleri wa dziko lino. Koma izizi sizinatheke chifukwa a Chakwera ndi anthu awo adabwera poyera kuti iwowo ayimanso pa udindo wa president, kusemphana ndi zomwe iwowo adalonjeza pomwe amakhazikitsa mgwirizanowu,” Mayi Joyce Banda kulakhurapo pa za m’gwirizano wa Tonse Alliance omwe sudatsatidwe mkomwe.
“A Chilima anali odabwa kwambiri ndi zomwe anthuwa adanena ndipo anabwera kuno kuzandifunsa kuti mamie onani zija mudasayina mu document mu kunjaku zikuwoneka ngati ndine onama koma inu munasayina, ndipo ine ndinayakha kuti eyadi ndinasayina ndithu,” anatero a Mayi Joyce Banda.
Malemu Saulos Chilima adamwalira pa 10 June 2024 pa ngozi ya ndenge ndi anthu ena asanu ndi atatu ku Chikangawa, pamene ankapita ku maliro a a Ralph Kasambala.
0 Comments