
M’tsogoleri wakale wadziko lino mayi Joyce Banda, wati iyenso ali ndi mafunso ochuluka zedi pa zomwe zinachitika pa tsiku lomwe wachiwiri wakale wa m’tsogoleri wa dziko lino malemu Saulos Chilima anafa pa ngozi ya ndege ndi anthu ena 8 ku Chikangawa.
Polakhura pa kanema wa Zodiak mayi Banda wati position ya Mayi Mary Chilima pa imfa ya Saulos ndi position yawonso, ndipo sakusintha.

“Ineyo ndinene pano kuti mafunso anga pa zomwe zinachitika pa 10 June 2024 sanayankhidwe ndipo sindikudziwa kuti nkumaganiza zotani,” iwo anatero.
Pa zomwe commission of inquiry inatulutsa, mayi Banda anati report ya commission inali yosamveka, ndipo inangobweletsanso mafunso ochuluka.
“The commission of inquiry was contradicting itself, so ineyo sindikudziwatu choti ndiganize zomwe tinawuzidwa ndi zomwe zinachitika sizikugwirizana. Ineyo bwanji mungondisiya chifukwa sindikudziwa ineyo sine wa za sayansi, sinenso pathologist kuti ndidziwe kuti munthu amatha kufera mwamba ndiye akamafika pansi amakhala opanda magazi, magazi amakhala thupi mulibe.”
“Sindikudziwa kuti ndi ndani angandifotokozere zonsezi so am dealing with too much,” iwo anatero akuwonetsa nkhope yokhumudwa komanso ya chisoni kwambiri.
Iwo anapitiliza kunena kuti mafunso ndi ochuluka zedi chifukwa anamva kuti ndege inafika ku Mzuzu, ndipo sinatere chifukwa cha nyengo yosakhala bwino. Ndiye Pilot anawuzidwa kuti abwelere ku Lilongwe.
“Komatu Pilot yo anakatha kupita ku Karonga komwe kunali kufupi komanso kunalibe fog. Komanso report yo ikubwera ndikumati ndege sinakafike ku Mzuzu, timu yomwe imafufufuza ndege inapita kumalo komwe sikunali ndege koma ndege inakapezeka popanda ndi mitengo yomwe chonde amayi ndisiyeni ine am dealing with too much,” iwo anatero.
0 Comments