M’busa wina mu nzinda wa Lilongwe wamwalira pamene analowa mu m’tsinje wa Bua kuti azibatize yekha.
Zadziwika kuti m’busayu dzina lake ndi Chisomo Duncan wa mpingo wa Ziyoni ndipo anapita kukabatiza nkhosa zake mu mtsinje wu.
Malingana ndi zomwe otsatira a mpingowu adauza mneneri wa polisi m’chigawo chapakati chakunzambwe, a Foster Benjamin, m’busayu atamaliza kubatiza nkhosa zake, analowanso m’madzimo kuti azibatize yekha ndipo sadatulukemonso.
Ntchito yosaka m’busayu idayambika pomwe idatenga masiku awiri ndipo nthupi lake lidapezeka. Pakali pano thupi la malemuwa lili pachipatala cha Malembo komwe achipatala ati m’ busayu wafa chifukwa chobanika.
0 Comments