Mayi Malita Kalirani a dzaka 66 awakwidzinga chifukwa chowaganizira kuti apha amayi awo a Nadimba Kalirani a zaka 82 powaphwanya ndi hamala ku Dowa.
M’neneli wa apolisi m’boma la Dowa, a Alice Sitima watsimikiza nkhaniyi ponena kuti zoopsyazi zachitika m’dera la lavu pa 08 December 2024, 10 koloko usiku.
Apolisi ati mayiyu ataledzera mowa wake wa kachasu pofika kunyumba kwawo anayamba kumenya mayi ake a Nadimba ndi hamala komanso chitsulo china m’mutu.
Anthu a m’mudzi atathamangira kunyumbako pakumva kulira, ndi pomwe gogoyu anaulura kuti mwana wake ndi amene wamumenya ndi hamala komanso chitsulo.
Gogo Nadimba atafika nawo ku chipatala ndi pomwe zotsatira zinawonetsa kuti amwalira kamba kovulala kwambiri m’mutu ndi nthiti.
0 Comments