
Pomwe namondwe otchedwa Jude wayandikira kulowa m’dziko muno kuchoka ku gombe la Nampula m’dziko la Mozambique, a Malawi amene tikukhala m’madera okhudzidwa maka mchigawo chakum’mwera, tiyeni tikhale osamala chifukwa pamapeto pa zonsezi, pali chiyembekezo kuti zonse zikhala bwino.
Anthu amene tikukhala m’phepete mwa mitsinje, tiyeni tisamuke ndikukakhala m’malo omwe ndi otetezedwa ku namondweyu. Nkutheka timaolokanso mitsinje, tioloke pa nthawi yokhayo yomwe mitsinjeyi sinadzadze ndi madzi.
Kwa tonse omwe tili ndi ziweto komanso katundu, tisathamangire kupulumutsa zimenezi pomwe madzi afika mkhosi chifukwa ndi zotheka kubwezeretsa ziweto ndi katundu pomwe moyo wathu ulibe sipeyala ndipo ngati muli ndi kuthekera, samutsilanitu ziweto ndi katundu wanu mwansangansanga.
Kwa anzathu amene timakhaka kufupi ndi mapiri m’madera amene namondweyu akhudze, tisamukire kwabwino kuti tipulumutse miyoyo.
Tisagone mnyumba zimene zafewa chifukwa chakuchuluka kwa mvulayi ndipo tionetsetse kuti malo amene tikukhala, ndiotetezeka ku nyengo imeneyi.
Namondwe ndi owopsa koma ndizotheka ndithu kupulumutsa miyoyo yathu ngati titapanga zinthu zoyenera. Musakhale ndi mantha, awa si mathero a dziko, khalani ndi chiyembekezo ndipo pangani zoyenera pamene mphepoyi ikuyembekezeka kulowa mchigawo chakum’mwera.
0 Comments