Mtumiki wa Mulungu Apostle Clifford Kawinga yemwe ndi m’tsogoleri wa Salvation For all Ministries International, akupitiliza ntchito yothandiza anthu osowa maka pa nthawi ino yomwe njala yafika posautsa m’dziko muno.
A Kawinga dzulo apereka matumba 2000 a chimanga kwa mabanja 2000 m’dera la GVH Masuku, m’boma la Chiradzulu omwe akhudzidwa ndi njala.
Iwowa anagawaso ma Baibulo ku mafumu 115 omwe anasonkhana pamalopo.
Mtumikiyu anagawaso mawu a Mulungu Kwa anthuwa ngati njira imodzi yofuna kupereka chimwemwe komanso chiyembekezo mu nyengo zowawa zomwe anthuwa akudutsamo.
Polakhura pa mwambowu, a Kawinga anati ndikofunika kwambiri kuti azitumiki a Mulungu adzithandiza ovutika maka pa nyengo ino yomwe njala yafika posautsa m’dziko muno.
Iwo anati kupereka ndi mbali ya chikhiristu ndipo iwo ngat Ministry amayika patsogolo mbali zonse zitatu zomwe ndi thupi, moyo, ndi mzimu.
“M’malawi muno, madera ambiri muli njala, njala imeneyi ikufunika ife azitumiki a Mulungu tigwirane manja tiafikire anthu tiwapulumutse chifukwa mpingo umakhala mpingo ukakhala ndi anthu a moyo timalalalikira kwa anthu a moyo osati akufa. Ndiye pachifukwa ichi tiyen tipitilize kuthandiza anthuwa monga ife tichitiramu,” iwo anatero.
Mfumu Masuku inayamikira a Kawinga pobwera ndi thandizo la ufa omwe uthandize anthu omwe akhala akusowa chakudya mu deralo.
Iwo anatinso ndi osangalala kwambiri malinga ndi mwambo wa mapemphero omwe unachitika chifukwa zawapangitsa kukhala a chiyembekezo.
“Kuno njala ndi yaikulu kwambiri chifukwa choti anthu sanakolole kamba kakuti mvula sinagwe bwino. Kunali dzuwa ndipo anthu pakadali pano akudya mango kuwaphika ngati phala ndikumadya. Kuti adye chakudya chenicheni ngati nsima akumatenga masiku awiri pena atatu,” iwo anatero.
0 Comments