Malawi News

Anthu anayi anjatidwa kamba kokhudzidwa pa imfa ya bambo wina

Anthu anayi anjatidwa kamba kokhudzidwa pa imfa ya bambo wina

Anthu anayi omwe ndi a Augustine Mahipo azaka 17, a Allan Tawakali azaka 31, a Julius Makina azaka 20 komanso a Emmanuel Misoya azaka 20, ali mmanja mwa apolisi ku Zomba powaganizira kuti anapha bambo wa zaka 85, a Yohane Chimwala.


Malingana ndi m’neneri wa polisi ya Zomba, a Patricia Sipiliano, anthuwa adachita izi usiku wa pa 20 January kudera la mfumu yaikulu Chikowi ku Zomba.


A Sipiliano anati anthuwa akuganizilidwa kuti anatenga zikwanje ndipo anapita kunyumba kwa a Chimwala komwe anakathyola nyumba nkuwakhapa malemuwo ndinso kuba ufa komanso wailesi ya Bluetooth.