Malawi News

Ana atatu afa atamira mu damu ku Dowa

Ana atatu afa atamira mu damu ku Dowa

Ana atatu omwe ndi a banja limodzi amwalira atamira pomwe amakasewera kufupi ndi damu lina m’boma la Dowa


Malingana ndi m’neneri wa polisi ya Mponela, a Macpatson Msadala, izi zachitika m’mudzi wa Chakomba mdera la mfumu yayikulu Chakhaza pa damu lomwe kalelo ankakumbamo miyala yokonzera mseu wa M1.


Sergeant Msadala ati izi zinachitika pamene makolo a anawo anapita kumunda ndipo atabwerako anawa sanawapezeze kunyumba.


Zitachitika izi anthu m’mudzimo anayamba kusaka anawa ndipo anapeza matupi awo akuyandama mu damu lo.