Malawi News

A Usi ayendera ntchito yogawa phala

A Usi ayendera ntchito yogawa phala

Dzulo laliwisili, wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, a Michael Usi, adali m’boma la Dowa komwe adakayendera ntchito yopereka phala kwa ophunzira a pa sukulu ya pulaimale ya Changalu.


Ntchito yogawa phalayi imagwiridwa ndi bungwe la Mary’s Meals ndipo pakulankhula kwawo a Usi adati ngakhale chakudya chimalimbikitsa thanzi la munthu, komanso kulimbikira maphunziro, ndipofunikiranso kuti ophunzira akhale otetezedwa m’makomo, mnjira popita ku sukulu, komanso m’ma sukulu awo.


Mwa zina zowe zidachitika patsikuli, a Usi adathandizira kupeleka phala kwa ophunzira pa sukulu yi.


M’mawu awo, Nduna ya za Maphunziro, a Madalitso Kambauwa Wirima adati maphunziro akwera tsopano kamba kakubwera kwa program yogawa phala m’masukulu ndipo ntchitoyi ikulimbikitsa ophunzira kuchita bwino m’kalasi,  kuchepetsa kujomba komanso kusiira sukulu pa njira.


Source: Dowa District Council