Nduna ya zamasewero a Uchizi Mkandawire yati mabwalo a masewero awiri omwe boma likumanga Ku Soche ndi Zingwangwa Ku Blantyre adzakhala a boma.
Poyamba mabwalowa adapelekedwa Ku Mighty Mukuru Wanderers komanso FCB Nyasa Big Bullets.
Koma polankhula mu nyumba ya malamulo Lolemba a Mkandawire ati mabwalowa adzakhala a boma ndipo kuti matimuwa adzasainila mgwirizano ndi boma ogwiritsa ntchito malowa.
Ndunayi inati kumangidwa Kwa bwalo la Soche kunayamba mu chaka cha 2019, Koma kunayimitsidwa kaye ndipo ntchitoyi inayambaso mu Chaka cha 2023.
“Kupitilila kwa ntchito yomanga mabwalo a masewero a Zingwangwa ndi Soche ku Blantyre kuyambika posachedwa. Ndondomeko zonse zili mchimake ndipo Ngati Boma tikuyembekeza kuti ndalama zomangila malowa zipezeka,” anatero a Mkandawire.
Malinga ndi a Mkandawire, kampani yomwe imamanga bwalo la Zingwangwa yavomela kuthetsa m’gwirizano wake ndi boma kaamba ka nkhani za mitengo ndipo undunawu uli mkati moyang’ana kontilakita wina.
Polakhulapo pa nkhaniyi phungu wa kumpoto kwa Kasungu a Mike Bango, anafunsa ndunayi ngati kuli kotheka kuti boma lingopeleka ma stadium wa ku ma timu awiriwa.
Mu Chaka cha 2019 m’tsogoleri wakale wa dziko lino a Peter Muntharika analonjeza Kuti Boma imanga ma bwalo a zamasero a matimu a Nyasa Big Bullets ndi Mighty Mukuru Wanderers.
A Mkandawire anawuzanso Nyumba ya Malamuloyi kuti ntchito yomanga malo a zamasewero a Griffin Sayenda ndi Aquatic Sports Center ku Lilongwe ziyambika ndondomeko ya chuma ya chaka chino isanathe.
Iwo anati ntchito zomanga malowa zinaima mu 2022 kaamba ka kukwera mitengo kwa katundu ndipo boma limadikira kuti nthambi yowona zogula ndi kugulitsa katundu wa boma iuwnike mitengoyo isadapereke chilorezo.
“Chilorezo chinaperekedwa mu July chaka chino ndipo ndalama zomangira malo a Griffin Sayenda zinachoka pa K7 billion kufika pa K15.3 billion pomwe Aquatic stadium ndalama yake inafika pa K8.2 billion kufika pa K14.2 billion,” anatero a Mkandawire.
0 Comments